1Inu Mulungu musakhale chete;
2Onani adani anu akuchita chiwawa,
3Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu;
4Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu
5Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu;
6Matenti a Edomu ndi Aismaeli,
7Agebala, Aamoni ndi Aamaleki,
8Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo
9Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani,
10Amene anawonongedwa ku Endori
11Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu
12amene anati, “Tiyeni tilande dziko
13Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga,
14Monga moto umatentha nkhalango,
15kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho,
16Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi
17Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse;
18Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova,