1Inu Yehova, mwandisanthula
2Inu mumadziwa pamene ndikhala pansi ndi pamene ndidzuka;
3Mumapenyetsetsa pamene ndikutuluka ndi kugona kwanga;
4Mawu asanatuluke pa lilime langa
5Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo komwe;
6Nzeru zimenezi ndi zopitirira nzeru zanga,
7Kodi ndingapite kuti kufuna kuzemba Mzimu wanu?
8Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko;
9Ngati ndiwulukira kotulukira dzuwa,
10kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera,
11Ndikanena kuti, “Zoonadi, mdima udzandibisa ndithu
12komabe mdimawo sudzakhala mdima kwa Inu;
13Pakuti Inu munalenga za mʼkati mwanga;
14Ndimakuyamikani chifukwa ndinapangidwa mochititsa mantha ndi modabwitsa;
15Mapangidwe anga sanabisike pamaso panu
16Maso anu anaona thupi langa lisanawumbidwe.
17Zolingalira zanu pa ine ndi zamtengowapatali, Inu Mulungu,
18Ndikanaziwerenga,
19Ndi bwino mukanangopha anthu oyipa, Inu Mulungu!
20Amayankhula za Inu ndi zolinga zoyipa;
21Kodi ine sindidana nawo amene amakudani, Inu Yehova?
22Ndimadana nawo kwathunthu;
23Santhuleni, Inu Mulungu ndipo mudziwe mtima wanga;
24Onani ngati muli mayendedwe aliwonse oyipa mwa ine,