1Mwana wanga, ngati wamuperekera mnansi wako chikole,
2ngati wagwidwa ndi zimene iwe unanena,
3Tsono popeza iwe mwana wanga
4Usagone tulo,
5Dzipulumutse monga imachitira mphoyo mʼdzanja la mlenje,
6Pita kwa nyerere, mlesi iwe;
7Zilibe mfumu,
8komabe zimasungiratu chakudya chake nthawi ya chilimwe
9Kodi uzingogonabe pamenepo mpaka liti mlesi iwe?
10Ukati ndingogona pangʼono, ndingowodzera pangʼono
11umphawi udzakugwira ngati mbala
12Munthu wachabechabe, munthu woyipa,
13amatsinzinira maso ake,
14amalingalira zoyipa ndi mtima wake wachinyengo
15Nʼchifukwa chake tsoka lidzamugwera modzidzimutsa;
16Pali zinthu zisanu ndi chimodzi zimene Yehova amadana nazo,
17maso onyada,
18mtima wokonzekera kuchita zoyipa,
19mboni yonama yoyankhula mabodza
20Mwana wanga, usunge malamulo a abambo ako;
21Zimenezi uzimatirire pa mtima pako masiku onse,
22Ukamayenda, zidzakulozera njira;
23Paja malamulo awa ali ngati nyale,
24kukupulumutsa kwa mkazi wadama,
25Mu mtima wako usakhumbire kukongola kwake,
26paja mkazi wadama amakusandutsa kukhala ngati nyenyeswa za buledi
27Kodi munthu angathe kutenga moto
28Kodi munthu angathe kuyenda pa makala amoto
29Ndizo zimachitikira munthu amene amagonana ndi mkazi wa munthu wina.
30Paja anthu sayinyoza mbala ikaba
31Komabe ngati mbalayo igwidwa iyenera kulipira kasanu nʼkawiri,
32Munthu wochita chigololo ndi wopanda nzeru.
33Adzalandira mabala ndi mʼnyozo,
34Paja nsanje imachititsa mwini mkaziyo kukalipa,
35Iye savomera dipo lililonse;