1Nawa mawu a Aguri mwana wa Yake wa ku Masa:
2“Ine ndine munthu wopusa kuposa anthu onse;
3Sindinaphunzire nzeru,
4Kodi ndani anakwera kumwamba ndi kutsikako?
5“Mawu ali wonse a Mulungu ndi opanda cholakwika;
6Usawonjezepo kanthu pa mawu ake,
7“Inu Yehova, ndikukupemphani zinthu ziwiri
8Choyamba, mundichotsere kutali nane mabodza ndi chinyengo.
9kuopa kuti ndikakhuta kwambiri ndingayambe kukukanani,
10“Usamusinjirire wantchito kwa mbuye wake
11“Alipo ena amene amatemberera abambo awo,
12Pali ena amene amadziyesa okha oyera mtima
13Pali ena ndi odzitukumula kwambiri,
14Pali ena amene mano awo ali ngati malupanga
15“Msundu uli ndi ana aakazi awiri
16Manda, mkazi wosabala,
17Aliyense amene amanyoza abambo ake,
18Pali zinthu zitatu zimene zimandidabwitsa,
19Ndipo ndi izi: mmene chiwulukira chiwombankhanga mlengalenga;
20Umu ndi mʼmene mkazi amachitira atachita chigololo:
21Pali zinthu zitatu zimene zimanjenjemeretsa dziko lapansi,
22Kapolo amene wasanduka mfumu,
23mkazi wonyozeka akakwatiwa
24Pali zinthu zinayi zingʼonozingʼono pa dziko lapansi,
25Nyerere zili ngati anthu opanda mphamvu,
26mbira zili ngati anthu opanda mphamvu
27dzombe lilibe mfumu,
28Buluzi ungathe kumugwira mʼmanja
29“Pali zinthu zitatu zimene zimayenda chinyachinya,
30Mkango umene uli wamphamvu kuposa nyama zonse,
31Tambala woyenda chinyachinya, mbuzi yayimuna,
32“Ngati wakhala ukupusa ndi kumadzikweza wekha,
33Paja pakutha mkaka mafuta amapangidwa,