1Mwana wanga, usayiwale malangizo anga,
2Ukatero zaka za moyo wako zidzachuluka
3Makhalidwe ochitira ena chifundo ndi owonetsa kukhulupirika asakuchokere.
4Ukatero udzapeza kuyanja ndi mbiri yabwino
5Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse
6Pa zochita zako zonse uvomereze kuti Mulungu alipo,
7Usamadzione ngati wa nzeru.
8Ukatero thupi lako lidzakhala la moyo wabwino
9Uzilemekeza Yehova ndi chuma chako chonse;
10Ukatero nkhokwe zako zidzadzaza ndi zinthu zambiri,
11Mwana wanga usanyoze malangizo a Yehova,
12Paja Yehova amadzudzula amene amamukonda,
13Wodala munthu amene wapeza nzeru,
14pakuti phindu la nzeru ndi labwino kuposa la siliva,
15Nzeru ndi yoposa miyala yamtengowapatali;
16Mʼdzanja lake lamanja muli moyo wautali;
17Njira zake ndi njira zosangalatsa,
18Nzeru ili ngati mtengo wopatsa moyo kwa oyigwiritsitsa;
19Yehova anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru.
20Mwa nzeru zake Yehova anatumphutsa madzi kuchokera mʼnthaka
21Mwana wanga usunge nzeru yeniyeni ndi khalidwe lomalingarira zinthu bwino.
22Zimenezi zidzakupatsa moyo,
23Choncho udzayenda pa njira yako mosaopa kanthu,
24pamene ugona pansi, sudzachita mantha;
25Usaope tsoka lobwera mwadzidzidzi
26pakuti Yehova adzakulimbitsa mtima
27Usaleke kuchitira zabwino amene ayenera kulandira zabwino,
28Usanene kwa mnansi wako kuti,
29Usamukonzere chiwembu mnansi wako,
30Usakangane ndi munthu wopanda chifukwa
31Usachite naye nsanje munthu wachiwawa
32Pakuti Yehova amanyansidwa ndi munthu woyipa
33Yehova amatemberera nyumba ya munthu woyipa,
34Anthu onyoza, Iye amawanyoza,
35Anthu anzeru adzalandira ulemu,