1“Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze?
2Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo;
3Amalanda abulu a ana amasiye
4Amachotsa mʼmisewu anthu osauka,
5Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu,
6Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake,
7Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala;
8Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri
9Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere;
10Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala;
11Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa;
12Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda,
13“Pali ena amene amakana kuwala,
14Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka
15Munthu wachigololo amadikira chisisira;
16Mbala zimathyola nyumba usiku,
17Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera.
18“Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi;
19Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana
20Mayi wowabereka amawayiwala,
21Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana,
22Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake;
23Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka,
24Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso;
25“Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza