1Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:
2“Yuda akulira,
3Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.
4Popeza pansi pawumiratu
5Ngakhale mbawala yayikazi
6Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu
7Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,
8Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani
9Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,
10Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:
11Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.
12Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”
13Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”
14Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo.
15Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala.
16Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.
17“Awuze mawu awa:
18Ndikapita kuthengo,
19Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?
20Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu
21Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;
22Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,