1Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.”
2Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.
3Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti,
4“Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.”
5Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.
6Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.”
7Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.
8Pamenepo Yehova anandiwuza kuti,
9“Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
10Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu.
11Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
12“Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’
13Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu.
14Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”
15Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,
16Lemekezani Yehova Mulungu wanu
17Koma ngati simumvera,
18Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,
19Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa
20Tukula maso ako kuti uwone
21Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
22Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
23Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
24“Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
25Limeneli ndiye gawo lanu,
26Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
27Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu