1Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite!
2Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti,
3“Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga.
4Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.
5“Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu?
6Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova.
7Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo
8Ndinachulukitsa amayi awo amasiye
9Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka
10Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine,
11Yehova anati,
12“Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo,
13Anthu ako ndi chuma chako
14Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu
15Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse;
16Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino.
17Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera,
18Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha?
19Tsono Yehova anandiyankha kuti,
20Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba
21“Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa