We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Yobu 9

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Yobu 8 Yobu Yobu 10 →

1Ndipo Yobu anayankha kuti,

2“Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona.

3Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye,

4Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka.

5Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa,

6Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake

7Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala;

8Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba

9Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana,

10Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka,

11Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona;

12Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa?

13Mulungu sabweza mkwiyo wake;

14“Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji?

15Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe;

16Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera,

17Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho,

18Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso

19Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi!

20Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa;

21“Ngakhale ine ndili wosalakwa,

22Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti,

23Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi,

24Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa

25“Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro;

26Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja,

27Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga,

28ndikuopabe mavuto anga onse,

29Popeza ndapezeka kale wolakwa

30Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri

31mutha kundiponyabe pa dzala,

32“Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha,

33Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu,

34munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine

35Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo,

← Yobu 8 Yobu Yobu 10 →