1Ndinayangʼananso ndi kuona chipsinjo chimene chimachitika pansi pano:
2Ndipo ndinanena kuti akufa,
3Koma wopambana onsewa
4Ndipo ndinazindikira kuti ntchito zonse zolemetsa ndiponso ntchito zonse zaluso zimachitika chifukwa choti wina akuchitira nsanje mnzake. Izinso ndi zopandapake, nʼkungodzivuta chabe.
5Chitsiru chimangoti manja ake lobodo
6Nʼkwabwino kukhala ndi dzanja limodzi lodzaza uli pa mtendere,
7Ndinaonanso chinthu china chopanda phindu pansi pano:
8Panali munthu amene anali yekhayekha;
9Kukhala awiri nʼkwabwino kuposa kukhala wekha,
10Ngati winayo agwa,
11Komanso ngati anthu awiri agona malo amodzi, adzafunditsana.
12Munthu mmodzi angathe kugonjetsedwa,
13Wachinyamata wosauka koma wanzeru aposa mfumu yokalamba koma yopusa imene simvanso malangizo.
14Wachinyamatayo angathe kuchokera ku ndende ndi kudzakhala mfumu, kapena angathe kubadwa wosauka mʼdziko la mfumuyo.
15Ndipo ndinaona kuti iwo onse amene anakhala ndi moyo ndi kuyenda pansi pano anatsatira wachinyamatayo, amene anatenga malo a mfumu.
16Mfumu ikhoza kulamulira anthu osawerengeka, komabe itamwalira, palibe amene adzayamikire zomwe mfumuyo inachita. Izinso ndi zopandapake, nʼkungozivuta chabe.