1Chinthu chilichonse chili ndi nthawi yake,
2Nthawi yobadwa ndi nthawi yomwalira,
3Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa,
4Nthawi yomva chisoni ndi nthawi yosangalala,
5Nthawi yotaya miyala ndi nthawi yokundika miyala,
6Nthawi yofunafuna ndi nthawi yoleka kufunafuna,
7Nthawi yongʼamba ndi nthawi yosoka,
8Nthawi yokondana ndi nthawi yodana,
9Kodi wantchito amapeza phindu lanji pa ntchito yake yolemetsa?
10Ine ndinaona chipsinjo chimene Mulungu anayika pa anthu.
11Iye anapanga chinthu chilichonse kuti chikhale chabwino pa nthawi yake. Anayika nzeru zamuyaya mʼmitima ya anthu; komabe anthuwo sangathe kuzindikira zomwe Mulungu wachita kuyambira pa chiyambi mpaka chimaliziro.
12Ine ndikudziwa kuti palibenso kanthu kabwino kwa anthu kopambana kusangalala ndi kuchita zabwino pamene ali ndi moyo.
13Ndi mphatso ya Mulungu kwa munthu kuti azidya, azimwa ndi kumakondwera ndi ntchito zake zolemetsa.
14Ndikudziwa kuti chilichonse chimene Mulungu amachita chidzakhala mpaka muyaya; palibe zimene zingawonjezedwe kapena kuchotsedwa. Mulungu amazichita kuti anthu azimuopa.
15Chilichonse chimene chilipo chinalipo kale,
16Ndipo ndinaona chinthu chinanso pansi pano:
17Ndinalingalira mu mtima mwanga kuti;
18Ndinalingaliranso kuti, “Kunena za anthu, Mulungu amawayesa ndi cholinga choti awaonetse kuti iwo ali ngati nyama.
19Zimene zimachitikira munthu, zomwezonso zimachitikira nyama; chinthu chimodzi chomwecho chimachitikira onse: Monga munthu amafa momwemonso nyama imafa. Zonsezi zimapuma mpweya umodzimodzi omwewo; munthu saposa nyama. Zonsezi ndi zopandapake.
20Zonse zimapita kumodzimodzi; zonsezi zimachokera ku fumbi, ndipo zimabwereranso ku fumbi komweko.
21Kodi ndani amene amadziwa ngati mzimu wa munthu umakwera kumwamba, ndipo mzimu wa nyama umatsikira kunsi kwa dziko?”
22Kotero ndinaona kuti palibe chinthu chabwino kwa munthu kuposa kuti munthu azisangalala ndi ntchito yake, pakuti ichi ndiye chake chenicheni. Pakuti ndani amene angamubweretse kuti adzaone zimene zidzamuchitikira iye akadzamwalira?