We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Mlaliki 5

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Mlaliki 4 Mlaliki Mlaliki 6 →

1Uzisamala mayendedwe ako pamene ukupita ku nyumba ya Mulungu. Upite pafupi kuti ukamvetsere mʼmalo mopereka nsembe ya zitsiru zimene sizizindikira kuti zikuchita zolakwa.

2Usamafulumire kuyankhula,

3Kuchuluka kwa mavuto mu mtima kumabweretsa maloto oyipa,

4Pamene ulumbira kwa Mulungu usachedwe kukwaniritsa chimene walumbiracho. Iye sakondweretsedwa ndi chitsiru; kwaniritsa lumbiro lako.

5Kuli bwino kusalumbira kusiyana ndi kulumbira koma osakwaniritsa lumbirolo.

6Pakamwa pako pasakuchimwitse. Ndipo usanene kwa mthenga wa mʼNyumba ya Mulungu kuti, “Ndinalakwitsa polumbira.” Chifukwa chiyani ukufuna Mulungu akwiye ndi mawu ako ndiponso ntchito ya manja ako?

7Maloto ochuluka ndi mawu ochuluka ndi zinthu zopandapake. Kotero lemekeza Mulungu.

8Ngati uwona anthu osauka akuzunzika mʼdziko, ndiponso anthu ena akupsinja anzawo ndi kuwalanda ufulu wawo, usadabwe ndi zinthu zimenezi; pakuti woyangʼanira ali naye wina womuyangʼanira wamkulu, ndipo pamwamba pa awiriwa pali ena akuluakulu owaposa.

9Anthu onse amatengako zokolola za mʼminda: koma ndi mfumu yokha imene imapeza phindu la mindayi.

10Aliyense amene amakonda ndalama sakhutitsidwa ndi ndalamazo;

11Chuma chikachuluka

12Wantchito amagona tulo tabwino

13Ine ndinaona choyipa chomvetsa chisoni pansi pano:

14kapena chuma chowonongedwa pa nthawi yatsoka,

15Munthu anabadwa wamaliseche kuchokera mʼmimba mwa amayi ake,

16Izinso ndi zoyipa kwambiri:

17Masiku ake onse ndi odzaza ndi mdima,

18Tsono ndinazindikira kuti nʼchabwino ndi choyenera kuti munthu azidya ndi kumwa, ndi kukhutitsidwa ndi ntchito yake yolemetsa imene amayigwira pansi pano pa nthawi yake yochepa imene Mulungu amamupatsa, poti ichi ndiye chake.

19Komatu pamene Mulungu apereka chuma kwa munthu aliyense ndi zinthu zina, ndi kulola kuti akondwere ndi chumacho, munthuyo alandire chumacho ndi kusangalala ndi ntchito yake, imene ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.

20Munthu wotereyu saganizirapo za masiku a moyo wake, chifukwa Mulungu amamutanganidwitsa ndi chisangalalo cha mu mtima mwake.

← Mlaliki 4 Mlaliki Mlaliki 6 →