1Mawu a Yehova odzudzula dziko la Hadiraki
2ndiponso mzinda wa Hamati, umene ukuchita malire ndi dzikoli,
3Ndipo Turo anadzimangira linga;
4Taonani Ambuye adzamulanda chuma chakecho
5Mzinda wa Asikeloni udzaona zimenezi, nʼkuchita mantha;
6Mu Asidodi mudzakhala mlendo,
7Ndidzachotsa nyama ya magazi mʼkamwa mwawo,
8Koma Ine ndidzalondera Nyumba yanga
9Sangalala kwambiri, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni!
10Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efereimu
11Tsono kunena za iwe, chifukwa cha magazi a pangano lako ndi Ine,
12Bwererani ku malo anu otetezedwa, inu amʼndende achiyembekezo;
13Ndidzakoka Yuda monga ndimakokera uta wanga,
14Pamenepo Yehova adzaonekera kwa anthu ake;
15ndipo Yehova Wamphamvuzonse adzawateteza.
16Tsiku limenelo Yehova Mulungu wawo adzawapulumutsa
17Taonani chikoka ndi kukongola kwawo!