1Nʼchifukwa chiyani Yehova mwayima patali?
2Mwa kunyada kwake munthu woyipa asaka wofowoka,
3Iye amatamandira zokhumba za mu mtima wake;
4Mwa kunyada kwake woyipa safunafuna Mulungu;
5Zinthu zake zimamuyendera bwino;
6Iye amadziyankhulira kuti, “Palibe chimene chidzandigwedeze.
7Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi zoopseza;
8Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi,
9Amabisalira anthu ngati mkango pa zitsamba.
10Anthuwo amawapondaponda ndipo amakomoka;
11Iye amati mu mtima mwake, “Mulungu wayiwala,
12Dzukani Yehova! Onetsani dzanja lanu Inu Mulungu.
13Nʼchifukwa chiyani munthu woyipa amachitira chipongwe Mulungu?
14Komatu Inu Mulungu, mumazindikira mavuto ndi zosautsa,
15Thyolani dzanja la woyipitsitsa ndi la munthu woyipa;
16Yehova ndi Mfumu kwamuyaya;
17Mumamva Inu Yehova, zokhumba za osautsidwa;
18Kuteteza ana amasiye ndi oponderezedwa,