1Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati:
2“Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga
3Onetsa chamuna;
4“Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi?
5Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa!
6Kodi maziko ake anawakumba potani,
7pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi
8“Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa,
9pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake
10pamene ndinayilembera malire ake
11Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire
12“Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa,
13kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi
14Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo;
15Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa,
16“Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja
17Kodi anakuonetsapo zipata za imfa?
18Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa?
19“Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti?
20Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi?
21Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale!
22“Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana
23zimene ndazisungira nthawi ya mavuto
24Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani
25Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula,
26kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu,
27kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa
28Kodi mvula ili ndi abambo ake?
29Kodi madzi owundana anawabereka ndani?
30pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala,
31“Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi?
32Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake
33Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa?
34“Kodi iwe ungathe kulamula mitambo
35Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime?
36Kodi ndani anayika nzeru mu mtima,
37Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo?
38pamene fumbi limasanduka matope,
39“Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
40pamene ili khale mʼmapanga mwawo
41Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani