1“Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”
2Yehova akuti,
3Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,
4Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;
5Mudzalimanso minda ya mpesa
6Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula
7Yehova akuti,
8Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,
9Adzabwera akulira;
10“Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;
11Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo
12Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;
13Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.
14Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,
15Yehova akuti,
16Yehova akuti,
17Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”
18“Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,
19Popeza tatembenuka mtima,
20Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,
21“Muyike zizindikiro za mu msewu;
22Udzakhala jenkha mpaka liti,
23Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’
24Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa.
25Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”
26Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.
27“Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda.
28Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova.
29“Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti,
30Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.”
31“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
32Silidzakhala ngati pangano
33“Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
34Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,
35Yehova akuti,
36Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.
37Yehova akuti,
38“Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya.
39Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa.
40Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”