We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Yeremiya 18

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Yeremiya 17 Yeremiya Yeremiya 19 →

1Yehova anawuza Yeremiya kuti,

2“Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.”

3Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero.

4Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.

5Kenaka Yehova anandiwuza kuti,

6“Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya.

7Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga,

8ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira.

9Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu.

10Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.

11“Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’

12Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ”

13Yehova akuti,

14Kodi chisanu chimatha pa matanthwe

15Komatu anthu anga andiyiwala;

16Dziko lawo amalisandutsa chipululu,

17Ngati mphepo yochokera kummawa,

18Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”

19Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni;

20Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino?

21Choncho langani ana awo ndi njala;

22Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo

23Koma Inu Yehova, mukudziwa

← Yeremiya 17 Yeremiya Yeremiya 19 →