We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Yobu 32

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Yobu 31 Yobu Yobu 33 →

1Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama.

2Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga.

3Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa.

4Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo.

5Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima.

6Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati:

7Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula;

8Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu,

9Si okalamba amene ali ndi nzeru,

10“Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni;

11Ndadikira nthawi yonseyi,

12ineyo ndinakumvetseranidi.

13Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru;

14Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine,

15“Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso;

16Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano,

17Inenso ndiyankhulapo tsopano;

18Pakuti ndili nawo mawu ambiri,

19mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo,

20Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike;

21Sindidzakondera munthu wina aliyense,

22pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika,

← Yobu 31 Yobu Yobu 33 →