1Pali mgodi wa siliva
2Chitsulo amachikumba pansi,
3Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale,
4Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu,
5Nthaka, imene imatulutsa zakudya,
6miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake,
7Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi,
8Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo,
9Munthu amaphwanya matanthwe olimba,
10Amabowola njira mʼmatanthwewo;
11Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso,
12“Koma nzeru zingapezeke kuti?
13Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo;
14Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’
15Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri,
16Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri,
17Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi,
18Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe;
19Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi;
20“Kodi tsono nzeru zimachokera kuti?
21Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse,
22Chiwonongeko ndi imfa zikuti,
23Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko,
24pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi
25Iye atapatsa mphepo mphamvu zake,
26atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa
27pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake;
28Ndipo Iye anati kwa munthu,