1Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
2Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira.
3Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti
4Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.
5Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
6Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe.
7Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
8Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”
9Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa:
10Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;
11Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?”
12mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali,
13Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko,