We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Yesaya 19

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Yesaya 18 Yesaya Yesaya 20 →

1Uthenga onena za Igupto:

2“Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha;

3Aigupto adzataya mtima

4Ndidzawapereka Aigupto

5Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa,

6Ngalande zake zidzanunkha;

7ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo

8Asodzi adzabuwula ndi kudandaula,

9Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima,

10Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,

11Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru;

12Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti?

13Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru,

14Yehova wasocheretsa

15Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite,

16Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga.

17Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.

18Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.

19Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso.

20Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa.

21Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo.

22Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.

23Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi.

24Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi.

25Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”

← Yesaya 18 Yesaya Yesaya 20 →