1Yehova anandiyankhula kuti:
2“Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo.
3Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti,
4Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja;
5Anakupanga ndi matabwa
6Ndi mitengo ya thundu ya ku Basani
7Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako,
8Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako.
9Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako,
10“Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Puti
11Anthu a ku Arivadi ndi Heleki
12“Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
13“Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
14“Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.
15“Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.
16“Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
17“Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
18“Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari.
19Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.
20“Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.
21“Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
22“Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
23“Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda.
24Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
25“Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali
26Anthu opalasa ako amakupititsa
27Chuma chako, katundu wako, malonda ako,
28Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezeka
29Onse amene amapalasa sitima zapamadzi,
30Iwo akufuwula,
31Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe
32Akuyimba nyimbo
33Pamene malonda ako ankawoloka nyanja
34Koma tsopano wathyokera mʼnyanja,
35Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanja
36Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola.