We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

1 Mbiri 24

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← 1 Mbiri 23 1 Mbiri 1 Mbiri 25 →

1Magulu a ana a Aaroni anali awa:

2Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe.

3Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira.

4Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara.

5Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.

6Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.

7Maere woyamba anagwera Yehoyaribu,

8achitatu anagwera Harimu,

9achisanu anagwera Malikiya,

10achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi,

11achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa,

12a 11 anagwera Eliyasibu,

13a 13 anagwera Hupa,

14a 15 anagwera Biliga,

15a 17 anagwera Heziri,

16a 19 anagwera Petahiya,

17a 21 anagwera Yakini,

18a 23 anagwera Delaya,

19Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.

20Za zidzukulu zina zonse za Levi:

21Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake:

22Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti;

23Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.

24Mwana wa Uzieli: Mika;

25Mʼbale wa Mika: Isiya;

26Ana a Merari: Mahili ndi Musi.

27Ana a Merari:

28Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.

29Kuchokera kwa Kisi:

30Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti.

31Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.

← 1 Mbiri 23 1 Mbiri 1 Mbiri 25 →