We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Numeri 24

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Numeri 23 Numeri Numeri 25 →

1Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu.

2Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye

3ndipo ananena uthenga wake:

4uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,

5“Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,

6“Monga zigwa zotambalala,

7Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;

8“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto

9Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,

10Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka.

11Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”

12Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine,

13kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena?

14Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”

15Ndipo iye ananena uthenga wake nati,

16Uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,

17“Ndikumuona iye koma osati tsopano;

18Edomu adzagonjetsedwa;

19Wolamulira adzachokera mwa Yakobo

20Kenaka Balaamu anaona Aamaleki ndipo ananena uthenga wake uwu:

21Kenaka anaonanso Akeni ndipo ananena uthenga wake,

22komabe inu Akeni mudzawonongedwa,

23Ndipo ananenanso uthenga wina kuti,

24Sitima zapamadzi zidzabwera kuchokera ku madooko a Kitimu;

25Pamenepo Balaamu ananyamuka ndi kubwerera kwawo ndipo Balaki anapitanso njira yake.

← Numeri 23 Numeri Numeri 25 →