We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Ahebri 3

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Ahebri 2 Ahebri Ahebri 4 →

1Nʼchifukwa chake abale oyera mtima, amenenso munayitanidwa ndi kumwamba, lingalirani za Yesu amene ndi Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chikhulupiriro chimene timavomereza.

2Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamupatsa udindowo, monga momwe Mose anali wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.

3Yesu anapezeka woyenera kulandira ulemu waukulu kuposa Mose, monga momwemonso womanga nyumba amalandira ulemu waukulu kuposa nyumbayo.

4Pakuti nyumba iliyonse imamangidwa ndi munthu wina, koma amene anapanga zonse ndi Mulungu.

5Mose anali wokhulupirika monga mtumiki mʼnyumba yonse ya Mulungu, kuchitira umboni zimene zidzayankhulidwe mʼtsogolo.

6Koma Khristu ndi wokhulupirika monga mwana pa nyumba ya Mulungu. Ndipo ndife nyumba yake ngati tipitirire kulimbika mtima ndi kunyadira zomwe tikuyembekerazo.

7Tsono monga Mzimu Woyera akuti,

8musawumitse mitima yanu

9Pamene makolo anu anandiputa ndi kundiyesa,

10Nʼchifukwa chake ndinawukwiyira mʼbadowo,

11Kotero Ine ndinalumbira nditakwiya kuti,

12Abale samalani, kuti pasapezeke wina aliyense mwa inu wokhala ndi mtima woyipa ndi wosakhulupirira, womulekanitsa ndi Mulungu wamoyo.

13Koma muzilimbikitsana tsiku ndi tsiku, ikanalipo nthawi imene imatchedwa kuti “Lero” kuti aliyense wa inu mtima wake usawumitsidwe ndi chinyengo cha tchimo.

14Pakuti timakhala anzake a Khristu, ngati tigwiritsitsa mpaka potsiriza chitsimikizo chimene tinali nacho pachiyambi.

15Monga kunanenedwa kuti,

16Nanga amene anamva ndi kuwukira anali ndani? Kodi si onse amene Mose anawatulutsa mu Igupto?

17Nanga amene Mulungu anawakwiyira zaka makumi anayi anali ndani? Kodi si anthu amene anachimwa, amene mitembo yawo inatsala mʼchipululu muja?

18Nanga Mulungu ankanena za ndani kuti sadzalowa mu mpumulo wake? Pajatu ankanena za anthu amene sanamvere aja.

19Tsono ife tikuona kuti sanalowe chifukwa cha kusakhulupirika kwawo.

← Ahebri 2 Ahebri Ahebri 4 →