We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Ahebri 10

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Ahebri 9 Ahebri Ahebri 11 →

1Malamulo ndi chithunzithunzi cha zinthu zabwino zimene zikubwera, osati madalitso enieniwo. Pa chifukwa chimenechi sizingatheke konse kuti nsembe zimodzimodzi, zoperekedwa kawirikawiri, kosalekeza ndi chaka ndi chaka, kuti nʼkusandutsa angwiro amene amabwera kudzapembedza.

2Ngati zikanamatero iwowo akanasiya kupereka nsembezo. Pakuti opembedzawo akanamayeretsedwa kamodzi kokha, sibwenzi chikumbumtima chawo chikuwatsutsabe chifukwa cha machimo awo.

3Koma nsembezo zimawakumbutsa anthuwo machimo awo chaka ndi chaka.

4Chifukwa nʼkosatheka kuti magazi angʼombe yayimuna ndi mbuzi yayimuna achotse machimo.

5Nʼchifukwa chake Khristu atabwera pa dziko lapansi anati,

6Simunakondwere nazo nsembe zopsereza

7Tsono, Ine ndinati, ‘Ndili pano Ine,

8Poyamba Iye anati, “Nsembe kapena zopereka zopsereza ndi nsembe zopereka chifukwa cha tchimo, Inu simunazifune kapena kukondwera nazo.” Ngakhale kuti Malamulo ndiye amanena kuti ziperekedwe.

9Pamenepo Iye anati, “Ndili pano Ine, ndabwera kudzachita zimene mukufuna.” Khristu anachotsa nsembe zoyamba zija kuti mʼmalo mwake ayikemo nsembe za mtundu wachiwiri.

10Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.

11Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo.

12Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu.

13Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake.

14Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.

15Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,

16“Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo

17Ndipo akutinso:

18Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.

19Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu.

20Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake.

21Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu.

22Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera.

23Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika.

24Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino.

25Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.

26Ngati ife tipitirira kuchimwa mwadala pamene tikudziwa choona, palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.

27Koma kumangodikira kokha ndi mantha chiweruzo ndiponso moto woopsa umene udzawononga adani a Mulungu

28Aliyense amene amakana malamulo a Mose amaphedwa popanda nʼchifundo chomwe, malingana pali mboni ziwiri kapena zitatu.

29Koposa kotani nanga ululu wachilango chimene adzalandire munthu amene amapeputsa Mwana wa Mulungu, amene amayesa magazi a pangano, amene anamuyeretsa, kukhala chinthu chodetsedwa, ndi kunyoza Mzimu wachisomo?

30Pakuti timadziwa amene anati, “Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.” Iye anatinso, “Ambuye adzaweruza anthu ake.”

31Nʼchinthu choopsa kugwa mʼmanja a Mulungu wamoyo.

32Kumbukirani masiku akale aja mutangowunikiridwa chatsopano, pa nthawi imeneyi munapirira zowawa zambiri.

33Nthawi zina ankakunyozani pagulu ndi kukuzunzani. Nthawi zina munkamva zowawa pamodzi ndi amene ankasautsidwa chotere.

34Munkawamvera chisoni amene anali mʼndende ndiponso munkalola mokondwera kuti akulandeni katundu wanu chifukwa munkadziwa kuti muli nacho chuma choposa ndi chosatha.

35Tsono musataye kulimbika mtima kwanuko pakuti mudzalandira nako mphotho yayikulu.

36Nʼkofunika kuti mupirire kuti pamene muchita chifuniro cha Mulungu mudzalandire zimene Iye analonjeza.

37Pakuti nʼkanthawi kochepa chabe,

38Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.

39Koma ife sindife amodzi a iwo obwerera mʼmbuyo mwa mantha ndi owonongedwa, koma ndife amodzi a amene akukhulupirira ndi wopulumutsidwa.

← Ahebri 9 Ahebri Ahebri 11 →