1Buku lofotokoza za mʼbado wa Yesu Khristu mwana wa Davide, mwana wa Abrahamu:
2Abrahamu anabereka Isake,
3Yuda anabereka Perezi ndi Zara, amene amayi awo anali Tamara.
4Aramu anabereka Aminadabu,
5Salimoni anabereka Bowazi amene amayi ake anali Rahabe,
6Yese anabereka Mfumu Davide.
7Solomoni anabereka Rehabiamu,
8Asa anabereka Yehosafati,
9Uziya anabereka Yotamu,
10Hezekiya anabereka Manase,
11Yosiya anali atabala Yekoniya ndi abale ake pamene Ayuda anatengedwa ukapolo kupita ku Babuloni.
12Ali ku ukapolo ku Babuloni,
13Zerubabeli anabereka Abiudi,
14Azoro anabereka Zadoki,
15Eliudi anabereka Eliezara,
16Yakobo anabereka Yosefe, mwamuna wa Mariya. Mariyayu ndiye anabereka Yesu wotchedwa Khristu.
17Kuyambira pa Abrahamu mpaka pa Davide, pali mibado khumi ndi inayi. Ndipo kuyambira pa Davide mpaka pamene Ayuda anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babuloni, pali mibado khumi ndi inayi. Ndiponso kuyambira nthawi ya ukapolo ku Babuloni mpaka pamene Khristu anabadwa, palinso mibado khumi ndi inayi.
18Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera.
19Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.
20Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera.
21Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”
22Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti,
23“Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”
24Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake.
25Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.