1Tsono Yobu anayankha kuti,
2“Achikhala mavuto anga anayezedwa,
3Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja;
4Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya,
5Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu,
6Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere,
7Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe;
8“Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha,
9achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye,
10Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi,
11“Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo?
12Kodi ine ndili ndi mphamvu?
13Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha,
14“Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka,
15Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga,
16Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja,
17koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe,
18Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi;
19Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi,
20Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi;
21Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza,
22Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake,
23ndilanditseni mʼdzanja la mdani,
24“Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete;
25Ndithu, mawu owona ndi opweteka!
26Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena,
27Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye
28“Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana.
29Fewani mtima, musachite zosalungama;
30Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga?