1Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti,
2“Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe?
3Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri,
4Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa;
5Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima,
6Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako?
7“Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse?
8Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa,
9Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu;
10Mikango imabangula ndi kulira,
11Mkango umafa chifukwa chosowa nyama,
12“Mawu anabwera kwa ine mwamseri,
13Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku,
14ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera
15Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga,
16Chinthucho chinayimirira
17‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu?
18Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe,
19nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi,
20Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa;
21Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu,