We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Yeremiya 22

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Yeremiya 21 Yeremiya Yeremiya 23 →

1Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti,

2‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi.

3Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano.

4Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo.

5Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ”

6Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi:

7Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge,

8“Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’

9Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”

10Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo;

11Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso.

12Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”

13“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo,

14Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu

15“Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri

16Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa,

17“Koma maso ako ndi mtima sizili penanso,

18Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti,

19Adzayikidwa ngati bulu,

20“Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko,

21Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere.

22Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse,

23Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni,

24“Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya.

25Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake.

26Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko.

27Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”

28Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka,

29Iwe dziko, dziko, dziko,

30Yehova akuti,

← Yeremiya 21 Yeremiya Yeremiya 23 →