1“Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga;
2Tsopano ndiyamba kuyankhula;
3Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama;
4Mzimu wa Mulungu wandiwumba,
5Mundiyankhe ngati mungathe;
6Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu;
7Musachite mantha ndipo musandiope ayi,
8“Koma inu mwayankhula ine ndikumva,
9‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo;
10Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo;
11Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo,
12“Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi,
13Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye
14Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana,
15Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku,
16amawanongʼoneza mʼmakutu
17kumuchotsa munthu ku zoyipa,
18kumulanditsa munthu ku manda,
19“Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake,
20kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya,
21Thupi lake limawonda
22Munthuyo amayandikira ku manda,
23“Koma patakhala mngelo ngati mthandizi,
24kudzamukomera mtima ndi kunena kuti,
25pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana;
26Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa.
27Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti,
28Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda,
29“Mulungu amachita zonsezi kwa munthu
30kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda,
31“Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere;
32Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni;
33Koma ngati sichoncho, mundimvere;