We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Yesaya 38

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Yesaya 37 Yesaya Yesaya 39 →

1Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”

2Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti,

3“Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.

4Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti:

5“Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako.

6Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.

7“ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza:

8Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.

9Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:

10Ine ndinaganiza kuti

11Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova,

12Nyumba yanga yasasuka

13Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa;

14Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba,

15Koma ine ndinganene chiyani?

16Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu.

17Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere

18Pakuti akumanda sangathe kukutamandani,

19Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,

20Yehova watipulumutsa.

21Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”

22Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”

← Yesaya 37 Yesaya Yesaya 39 →