1Ansembe ndi Alevi amene anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa anali awa:
2Amariya, Maluki, Hatusi,
3Sekaniya, Rehumu, Meremoti,
4Ido, Ginetoyi, Abiya
5Miyamini, Maadiya, Biliga,
6Semaya, Yowaribu, Yedaya,
7Salu, Amoki, Hilikiya ndi Yedaya.
8Alevi anali Yesuwa, Binuyi, Kadimieli, Serebiya, Yuda, ndiponso Mataniya, amene pamodzi ndi abale ake ankatsogolera nyimbo za mayamiko.
9Abale awo, Bakibukiya ndi Uri, ankayimba nyimbo molandizana.
10Yesuwa anabereka Yowakimu, Yowakimu anabereka Eliyasibu, Eliyasibu anabereka Yoyada.
11Yoyada anabereka Yonatani, ndipo Yonatani anabereka Yaduwa.
12Pa nthawi ya Yowakimu, awa ndiwo anali atsogoleri a mabanja a ansembe:
13wa fuko la Ezara anali Mesulamu;
14wa fuko la Maluki anali Yonatani;
15wa fuko la Harimu anali Adina;
16wa fuko la Ido anali Zekariya;
17wa fuko la Abiya anali Zikiri;
18wa fuko la Biliga anali Samuwa;
19wa fuko la Yowaribu anali Matenayi;
20wa fuko la Salai anali Kalai;
21wa fuko la Hilikiya anali Hasabiya;
22Pa nthawi ya Eliyasibu, Yoyada, Yohanani ndi Yaduwa panalembedwa atsogolera a mabanja a Alevi ndi a ansembe mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Dariyo Mperisi.
23Zidzukulu za Levi, makamaka atsogoleri a mabanja awo analembedwa mʼbuku la mbiri mpaka pa nthawi ya Yohanani mwana wa Eliyasibu.
24Ndipo atsogoleri a Alevi awa, Hasabiya, Serebiya, Yesuwa mwana wa Kadimieli ndi abale awo, ankayimba nyimbo zotamanda ndi zothokoza molandizana. Gulu limodzi linkavomerezana ndi linzake monga mmene Davide munthu wa Mulungu analamulira.
25Mataniya, Bakibukiya, Obadiya, Mesulamu, Talimoni ndi Akubu anali olonda nyumba zosungiramo chuma pa zipata za ku Nyumba ya Mulungu.
26Iwo ndiwo ankatumikira pa nthawi ya Yowakimu mwana wa Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndiponso pa nthawi ya bwanamkubwa Nehemiya ndi wansembe Ezara amene analinso mlembi.
27Pa mwambo wopereka khoma la Yerusalemu anayitana Alevi kulikonse kumene ankakhala kuti abwere ku Yerusalemu ku mwambo wopereka khoma kwa Mulungu, mwachimwemwe ndi mothokoza poyimba nyimbo pamodzi ndi ziwiya za malipenga, azeze ndi apangwe.
28Tsono anthu a mabanja a Alevi oyimba nyimbo aja anasonkhana pamodzi kuchokera ku madera onse ozungulira Yerusalemu ndiponso ku midzi ya Anetofati,
29Beti-Giligala ndi ku madera a ku Geba ndi Azimaveti, pakuti oyimbawo anali atamanga midzi yawo mozungulira Yerusalemu.
30Tsono ansembe ndi Alevi anachita mwambo wodziyeretsa. Pambuyo pake anachita mwambo woyeretsa anthu onse ndi khoma la Yerusalemu.
31Ine ndinabwera nawo atsogoleri a dziko la Yuda ndi kukwera nawo pa khoma. Ndipo ndinasankha magulu awiri akuluakulu oyimba nyimbo za matamando. Gulu limodzi linadzera mbali ya ku dzanja lamanja pa khoma mpaka ku Chipata cha Kudzala.
32Pambuyo pawo panali Hosayia, theka la atsogoleri a Yuda aja
33pamodzi ndi Azariya, Ezara, Mesulamu,
34Yuda, Benjamini, Semaya ndi Yeremiya.
35Ena mwa ana a ansembe amene ankayimba malipenga awo anali awa: Zekariya mwana wa Yonatani mwana wa Semaya mwana wa Mataniya, mwana wa Mikaya, mwana wa Zakuri, mwana wa Asafu,
36pamodzi ndi abale awo awa: Semaya, Azareli, Milalai, Gilalayi, Maayi, Netaneli, Yuda ndi Hanani. Onse ankagwiritsa ntchito zida zoyimbira za Davide, munthu wa Mulungu. Tsono Ezara mlembi uja ankawatsogolera.
37Kuchokera ku Chipata cha Kasupe anayenda nakakwera makwerero opita ku mzinda wa Davide pa njira yotsatira khoma, chakumtundu kwa nyumba ya Davide mpaka ku Chipata cha Madzi, mbali ya kummawa.
38Gulu loyimba lachiwiri linadzera mbali ya kumanzere kwa khomalo. Tsono ine ndi theka lina la atsogoleri aja tinkalitsata pambuyo tikuyenda pamwamba pa khomalo. Tinapitirira Nsanja ya Ngʼanjo mpaka ku Khoma Lotambasuka.
39Tinadutsanso Chipata cha Efereimu, Chipata cha Yesana, Chipata cha Nsomba, Nsanja ya Hananeli, Nsanja ya Zana mpaka kukafika ku Chipata cha Nkhosa. Ndipo mdipiti uwu unakayima pa Chipata cha Mlonda.
40Choncho magulu onse awiri oyimba nyimbo zothokoza aja anakayima pafupi ndi Nyumba ya Mulungu. Pamodzi ndi ine ndi theka la atsogoleri aja,
41panalinso ansembe awa akuyimba malipenga: Eliyakimu, Maaseya, Miniyamini, Mikaya, Eliyoenai, Zekariya ndi Hananiya.
42Panalinso ansembe awa: Maaseya, Semaya, Eliezara, Uzi, Yehohanani, Milikiya, Elamu ndi Ezeri. Gulu loyimba linkatsogozedwa ndi Yezirahayiya.
43Pa tsiku limenelo anthu anapereka nsembe zambiri ndipo anakondwera chifukwa Mulungu anawapatsa chimwemwe chachikulu. Nawonso akazi ndi ana anakondwera ndipo kukondwa kwa anthu a mu mzinda wa Yerusalemu kunamveka kutali.
44Tsiku limenelo panasankhidwa anthu oyangʼanira zipinda zosungiramo zopereka zaufulu, zipatso zoyamba kucha, zopereka za chakhumi. Anthuwo ankasonkhanitsa zopereka kuchokera ku minda ya midzi yonse kuti azipereke kwa ansembe ndi Alevi malingana ndi malamulo. Izi zinali chomwechi chifukwa Ayuda ankakondwera ndi utumiki wa ansembe ndi Alevi.
45Iwowa ankagwira ntchito ya Mulungu wawo, makamaka mwambo woyeretsa zinthu. Nawonso oyimba nyimbo ndi olonda ku Nyumba ya Mulungu anagwira ntchito zawo monga Davide ndi mwana wake Solomoni analamula.
46Pakuti kalekale, pa nthawi ya Davide ndi Asafu, panali atsogoleri a anthu oyimba nyimbo za matamando ndi nyimbo zoyamika Mulungu.
47Choncho mu nthawi ya Zerubabeli ndi Nehemiya, Aisraeli onse anakapereka mphatso tsiku ndi tsiku kwa anthu oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu. Ankayikanso padera chigawo cha zopereka cha Alevi. Nawonso Alevi ankayika padera chigawo cha zopereka cha ansembe, zidzukulu za Aaroni.