We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Genesis 10

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Genesis 9 Genesis Genesis 11 →

1Nayi mbiri ya ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Ana atatuwa anabereka ana awo chitatha chigumula.

2Ana aamuna a Yafeti anali:

3Ana aamuna a Gomeri anali:

4Ana aamuna a Yavani anali:

5(Amenewa ndiwo makolo a anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja. Awa ndi ana a Yafeti monga mwa mafuko a mu mitundu yawo, uliwonse ndi chiyankhulo chake).

6Ana aamuna a Hamu anali:

7Ana aamuna a Kusi anali:

8Kusi anabereka Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi.

9Iye anali mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova; nʼchifukwa chake anthu ali ndi chisudzo, chakuti, “Ndiwe mlenje wamphamvu kwambiri pamaso pa Yehova monga Nimurodi.”

10Malo oyambirira a ufumu wake anali Babeli, Ereki, Akadi ndi Kaline. Malo onsewa anali mʼdziko la Sinara.

11Atachoka mʼdziko limeneli anapita ku Asiriya kumene anakamanga Ninive, Rehoboti-Iri, Kala,

12ndi Reseni, mzinda waukulu umene uli pakati pa Ninive ndi Kala.

13Igupto ndiye kholo la

14Apaturusi, Akasilu ndi Akafitori (kumene kunachokera Afilisti).

15Kanaani anabereka mwana wake wachisamba,

16Ayebusi, Aamori, Agirigasi;

17Ahivi, Aariki, Asini,

18Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.

19mpaka ku malire a Kanaani. Malirewo anachokera ku Sidoni kulowa cha ku Gerari mpaka ku Gaza, ndi kulowa ku Sodomu, Gomora, Adima ndi Zeboimu mpaka ku Lasa.

20Amenewa ndiwo ana aamuna a Hamu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe amakhala ndi mitundu yawo.

21Semu amene anali mkulu wake wa Yafeti nayenso anabereka nakhala kholo la Eberi.

22Ana aamuna a Semu anali:

23Ana aamuna a Aramu anali:

24Aripakisadi anabereka Sela,

25A Eberi anabereka ana aamuna awiri:

26Yokitani anabereka

27Hadoramu, Uzali, Dikila,

28Obali, Abimaeli, Seba,

29Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.

30Chigawo chimene ankakhala chinayambira ku Mesa mpaka ku Seferi, ku dera la mapiri chakummawa.

31Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mafuko ndi ziyankhulo zawo, mʼmadera omwe ankakhala ndi mitundu yawo.

32Amenewa ndiwo mafuko a ana aamuna a Nowa monga mwa mibado ya mitundu yawo. Mitundu yonse ya anthu inatuluka mwa iwowa ndi kufalikira pa dziko lonse lapansi chitatha chigumula chija.

← Genesis 9 Genesis Genesis 11 →