We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Ezekieli 32

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Ezekieli 31 Ezekieli Ezekieli 33 →

1Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti:

2“Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,

3“Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,

4Ndidzakuponya ku mtunda

5Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri

6Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,

7Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba

8Zowala zonse zamumlengalenga

9Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri

10Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,

11“ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,

12Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe

13Ndidzawononga ziweto zake zonse

14Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake

15Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;

16“Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”

17Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti:

18“Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa.

19Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’

20Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo.

21Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’

22“Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo.

23Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.

24“Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda.

25Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.

26“Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo.

27Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.

28“Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.

29“Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.

30“Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.

31“Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.

32Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”

← Ezekieli 31 Ezekieli Ezekieli 33 →