1Yehova anandiyankhula kuti:
2“Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.
3Pakuti tsiku layandikira,
4Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto
5Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.
6“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:
7“ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja
8Nditatha kutentha Igupto
9“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
10“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
11Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja
12Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo
13“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
14Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,
15Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
16Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
17Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
18Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
19Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
20Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti:
21“Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga.
22Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake.
23Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri.
24Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo.
25Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto.
26Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”