We Believe JesusFé, Esperança e Nova Vida

Ezekieli 21

Biblica® Tsekulani Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero · nianja

← Ezekieli 20 Ezekieli Ezekieli 22 →

1Yehova anandiyankhula nati:

2“Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu.

3Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe.

4Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto.

5Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’

6“Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu.

7Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”

8Yehova anandiyankhulanso kuti,

9“Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti,

10Lanoledwa kuti likaphe,

11“ ‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe,

12Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu,

13“ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’

14“Tsono mwana wa munthu, nenera

15Ndawayikira pa zipata zawo zonse

16Iwe lupanga, ipha anthu kumanja,

17Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga,

18Yehova anandiyankhulanso kuti,

19“Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda.

20Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa.

21Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe.

22Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo.

23Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.

24“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.

25“ ‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni,

26Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa.

27Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’

28“Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti,

29Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza.

30“ ‘Bwezerani lupanga mʼchimake.

31Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu,

32Mudzakhala ngati nkhuni pa moto.

← Ezekieli 20 Ezekieli Ezekieli 22 →