1Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi:
2Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
3Yehova ndi wankhondo;
4Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo
5Nyanja yakuya inawaphimba;
6Yehova, dzanja lanu lamanja
7Ndi ulemerero wanu waukulu,
8Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu
9Mdaniyo anati,
10Koma Inu munawuzira mphepo yanu,
11Ndithu Yehova, pakati pa milungu,
12Munatambasula dzanja lanu lamanja
13Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera
14Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha,
15Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu,
16Onse agwidwa ndi mantha woopsa.
17Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa
18“Yehova adzalamula
19Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma.
20Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina.
21Miriamu anawayimbira nyimbo iyi:
22Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi.
23Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara).
24Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?”
25Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino.
26Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.”
27Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi.