1Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.
2Iwo anabwerera pamodzi ndi Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Seruya, Reelaya, Mordekai, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Baana).
3Zidzukulu za Parosi
4zidzukulu za Sefatiya
5zidzukulu za Ara
6zidzukulu za Pahati-Mowabu (zochokera kwa Yesuwa ndi Yowabu)
7zidzukulu za Elamu
8zidzukulu za Zatu
9zidzukulu za Zakai
10zidzukulu za Bani
11zidzukulu za Bebai
12zidzukulu za Azigadi
13zidzukulu za Adonikamu
14zidzukulu za Bigivai
15zidzukulu za Adini
16zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)
17zidzukulu za Bezayi
18zidzukulu za Yora
19zidzukulu za Hasumu
20zidzukulu za Gibari
21Anthu a ku Betelehemu
22Anthu aamuna a ku Netofa
23Anthu aamuna a ku Anatoti
24Anthu aamuna a ku Azimaveti
25Anthu aamuna a ku Kiriati Yearimu, Kefira ndi Beeroti
26Anthu aamuna a ku Rama ndi Geba
27Anthu aamuna a ku Mikimasi
28Anthu aamuna a ku Beteli ndi Ai
29Anthu aamuna a ku Nebo
30Anthu aamuna a ku Magaibisi
31Anthu aamuna a ku Elamu wina
32Anthu aamuna a ku Harimu
33Anthu aamuna a ku Lodi, Hadidi ndi Ono
34Anthu aamuna a ku Yeriko
35Anthu aamuna a ku Sena
36Ansembe anali awa:
37Zidzukulu za Imeri
38Zidzukulu za Pasuri
39Zidzukulu za Harimu
40Alevi anali awa:
41Anthu oyimba nyimbo anali awa:
42Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
43Otumikira ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
44zidzukulu za Kerosi, zidzukulu za Siyaha, Padoni,
45zidzukulu za Lebana, zidzukulu za Hagaba, zidzukulu za Akubu,
46zidzukulu za Hagabu, zidzukulu za Salimayi, zidzukulu za Hanani,
47zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari, zidzukulu za Reaya,
48zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nekoda, zidzukulu za Gazamu,
49zidzukulu za Uza, zidzukulu za Peseya, zidzukulu za Besai,
50zidzukulu za Asina, zidzukulu za Meunimu, Nefusimu,
51zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
52zidzukulu za Baziruti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
53zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema,
54zidzukulu za Neziya ndi zidzukulu za Hatifa.
55Zidzukulu za antchito a Solomoni zinali izi:
56zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
57zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu,
58Chiwerengero cha onse otumikira ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za Solomoni chinali
59Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
60Zidzukulu za Delaya, zidzukulu za Tobiya, ndi zidzukulu za Nekoda. Onse pamodzi anali
61Ndi ena pakati pa ansembe anali awa:
62Amenewa anafufuza mayina awo mʼbuku lofotokoza mbiri ya mafuko awo, koma mayinawo sanawapezemo, choncho anawachotsa pa unsembe ngati anthu odetsedwa pa zachipembedzo.
63Bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo mpaka atapezeka wansembe wodziwa kuwombeza ndi Urimu ndi Tumimu.
64Chiwerengero cha anthu onse pamodzi chinali 42,360,
65kuwonjezera pamenepo, panalinso antchito awo aamuna ndi aakazi okwanira 7,337. Analinso ndi amuna ndi akazi oyimba nyimbo okwanira 200.
66Anali ndi akavalo 736, nyulu 245,
67ngamira 435 ndi abulu 6,720.
68Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.
69Anapereka kwa msungichuma wa ntchitoyo molingana ndi mmene aliyense chuma chake chinalili: golide wa makilogalamu 500, siliva makilogalamu 2,800 ndi zovala za ansembe zokwanira 100.
70Ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda ndi antchito a ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmidzi ya makolo awo.