1Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero.
2Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:
3Pakuti mayiko onse amwa
4Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:
5pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,
6Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.
7Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri
8Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;
9“Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake.
10Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.
11“Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo,
12katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira;
13zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.
14“Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’
15Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro
16ndipo adzalira mokuwa kuti,
17Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’
18Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’
19Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,
20“Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!
21Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,
22Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,
23Kuwala kwa nyale
24Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,