1Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu.
2Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova.
3Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.
4Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli.
5Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga,
6ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.
7Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:
8Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
9Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;
10Nyadirani dzina lake loyera;
11Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
12Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita,
13inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake,
14Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
15Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse,
16pangano limene anachita ndi Abrahamu,
17Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo,
18“Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani
19Ali anthu owerengeka,
20iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,
21Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze;
22“Musakhudze odzozedwa anga;
23Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi;
24Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse,
25Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
26Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake,
27Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake;
28Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,
29perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.
30Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi!
31Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere;
32Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
33Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba,
34Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;
35Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,
36Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli,
37Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse.
38Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.
39Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni
40kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli.
41Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
42Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.
43Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.